27/02/2026
Anthu okonda kusangalala m'boma la Mulanje ndi maboma ozungulira mawa, Loweruka, kopita kwawo ndi ku Cork and Bottle komwe kuli phwando la maimbidwe.
Katswiri woimba, Teddy Makadi, atsogolera chikondwererochi ndi nyimbo zake monga M'malele, Misala, Chulu, Nawe, Naliyera and Uziutenga.
Mmodzi mwa okonza msangulutsowo, katswiri wosewera nyimbo, MQ The DJ, wati chilichonse chili m'chimake kuti anthu asangalalire chikondi mothetsa mankhalu mawali.
Naye Teddy analemba pa tsamba lake Facebook kutsimikiza za kupezeka kwake ku malowa omwe ali kuseli kwa bwalo la za masewero la Mulanje Park.
Zina zochitika pa tsikuli ndi monga mayere, kuzipenta nkhope, kuwonera masewero a mpira, ndi kumwa zakumwa zaukali.
Wolemba: Temwa Mhone-Correspondent