19/05/2025
Ngongole ya feteleza alimi kuwadura 93% ngati adatenga mokuba??
Atsogoleri amene muli ku Sukambizi pepani zikadakhala bwino mukadawapedzera alimiwa Bank or Organization iliyonse imene ingamakwanise kumawabwereka zipangizo monga fetereza ndi zina zotere. Ngati izi zingakukanikeni ndiye apatseni mpata alimiwa kuti apange Organization yawo ndicholinga choti azikwanitsa kupeza zipangizozi pangongole mosavuta.
Izi zachitikazi mbambadi nkupha kwenikweni. Sizidachitikepo ngongole kudura 93%. Mumati alimiwa antchito awo awalipira ndichani? Alimiwa aduridwa 93% bwanji atsogoleri a Sukambizi mwakhala chete?? Tsoka nkukhalanso kuti ana anali akubwelera ku sukulu, mumati school fees akatenge kuti??